2 Chronicles 22:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo adatsatanso uphungu wao, ndipo adapita pamodzi ndi Yoramu, mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israele, kuti akamenyane nkhondo ndi Hazaele, mfumu ya ku Siriya, ku Ramoti ku Giliyadi. Kumeneko Asiriya adamlasa Yoramu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anayendanso m'kupangira kwao, namuka pamodzi ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, kukayambana nkhondo ndi Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndipo Aaramu anamlasa Yehoramu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyeyo anatsatiranso uphungu wawo pamene anapita ndi Yehoramu, mwana wa Ahabu, mfumu ya Israeli kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yehoramu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anayendanso m'kupangira kwao, namuka pamodzi ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israyeli, kukayambana nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Gileadi; ndipo Aaramu anamlasa Yehoramu.