2 Chronicles 22:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iye adabwerera napita ku Yezireele kuti akamchiritse mabala amene adaamlasa ku Rama, pamene ankamenyana ndi Hazaele mfumu ya ku Siriya. Motero Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda adapita ku Yezireele kukazonda Yoramu, mwana wa Ahabu, chifukwa chakuti ankadwala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nabwerera iye kuti amchize ku Yezireele, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaele mfumu ya Aramu. Ndipo Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu m'Yezireele, popeza anadwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kotero iye anabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene anamuvulaza ku Ramoti pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aaramu. Ndipo Ahaziya, mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anapita ku Yezireeli kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu chifukwa anavulazidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nabwerera iye kuti amcize ku Yezreeli, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaeli mfumu ya Aramu, Ndipo Azariya mwana wa Yehoramu mfumu yaYuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu m'Yezreeli, popeza anadwala.