2 Chronicles 22:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Mulungu adazikonzeratu kuti Ahaziya aonongedwe pokacheza kwa Yoramuyo. Atafika kumeneko, adapita pamodzi ndi Yoramu kuti akakumane ndi Yehu, mwana wa Nimisi, amene Chauta adaamsankha kuti aononge banja la Ahabu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehoramu; pakuti atafika anatulukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anakonza kuti Ahaziya akaphedwe pa ulendo wake wokacheza. Ahaziya atafika, iye ndi Yoramu anapita kukakumana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamudzoza kuti akawononge banja la Ahabu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehocamu; pakuti atafika anaturukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimsi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu.