2 Chronicles 22:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adafunafuna Ahaziya, ndipo adamgwira pamene ankabisala ku Samariya. Adabwera naye kwa Yehu, namupha. Anthuwo adamuika m'manda, poti ankati, “Ameneyu ndi mdzukulu wa Yehosafati uja amene ankatumikira Chauta ndi mtima wake wonse.” Choncho banja la Ahaziya linalibe munthu woti nkukhala mfumu yomalamulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala m'Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wake wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anapita kukafunafuna Ahaziya, ndipo anthu ake anagwira Ahaziya pamene amabisala mu Samariya. Anabwera naye kwa Yehu ndipo anaphedwa. Iwo anamuyika mʼmanda, pakuti anati, “Iyeyu anali mwana wa Yehosafati amene anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.” Kotero panalibe wamphamvu mʼbanja la Ahaziya kuti nʼkukhala mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala m'Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wace wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo.