2 Chronicles 23:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, wansembe Yehoyada adalimba mtima, naitana anthu aŵa, amene anali atsogoleri a anthu mazana: Azariya, mwana wa Yerohamu, Ismaele mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseiya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anadzilimbitsa natenga atsogoleri a mazana, Azariya mwana wa Yerohamu, ndi Ismaele mwana wa Yehohanani, ndi Azariya mwana wa Obedi, ndi Maaseiya mwana wa Adaya, ndi Elisafati mwana wa Zikiri, apangane naye pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaonetsa mphamvu zake. Iye anachita pangano ndi olamulira magulu a anthu 100: Azariya mwana wa Yerohamu, Ismaeli mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma caka cacisanu ndi ciwiri Yehoyada anadzilimbitsa natenga atsogoleri a mazana, Azariya mwana wa Yeroamu, ndi Ismayeli mwana wa Yohanana, ndi Azariya mwana wa Obedi, ndi Maaseya mwana wa Adaya, ndi Elisafati mwana wa Zikiri, apangane naye pamodzi.