2 Chronicles 23:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adandanditsa anthu onsewo kuti aziteteza mfumu, aliyense ali ndi mkondo m'manja, kuyambira kumwera kwa Nyumbayo mpaka kumpoto kwake, pafupi ndi guwa mpaka pa khomo la Nyumba kuti azizungulira mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaika anthu onse, yense ndi chida chake m'dzanja lake, amzinge mfumu, kuyambira mbali ya kudzanja lamanja la nyumba kufikira mbali ya kudzanja lamanzere la nyumba, kuloza kuguwa la nsembe ndi kunyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayika anthu onse, aliyense ali ndi chida mʼdzanja lake mozungulira mfumu pafupi ndi guwa ndi Nyumba ya Mulungu, kuyambira mbali ya kummwera mpaka kumpoto kwa Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaika anthu onse, yense ndi cida cace m'dzanja lace, amzinge mfumu, kuyambira mbali ya ku dzanja lamanja la nyumba kufikira mbali ya ku dzanja lamanzere la nyumba, kuloza ku guwa la nsembe ndi kunyumba.