2 Chronicles 23:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adaŵatulutsira mwana wa mfumu, namuveka chisoti chaufumu, nkumupatsa buku la malamulo, ndipo adamlonga ufumu. Tsono Yehoyada pamodzi ndi ana ake adamdzoza, anthu nafuula kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anatulutsa mwana wa mfumu, namveka korona, nampatsa mboni, namlonga ufumu; ndi Yehoyada ndi ana ake anamdzoza, nati, Ikhale ndi moyo mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehoyada ndi ana ake anatulutsa mwana wa mfumu ndipo anamumveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano namulonga ufumu. Yehoyada ndi ana ake anamudzoza ndipo anafuwula kuti, “Ikhale ndi moyo wautali mfumu!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anaturutsa mwana wa mfumu, nambveka korona, nampatsa mboni, namlonga ufumu; ndi Yehoyada ndi ana ace anamdzoza, nati, Ikhale ndi moyo mfumu.