2 Chronicles 23:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atayang'ana, adaona mfumu itaima pa nsanja yake pa khomo, atsogoleri ndi anthu oimba malipenga ali pafupi ndi mfumuyo. Anthu onse am'deralo ankakondwa, namaimba malipenga. Anthu oimba nyimbo ali ndi zipangizo zao zoimbira, ndiwo amene ankatsogolera chikondwererocho. Pamenepo Ataliyayo adang'amba zovala zake ndipo mofuula adati, “Akundiwukira! Akundiwukira!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yake polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m'dziko anakondwera, naomba amalipenga; oimbira omwe analiko ndi zoimbirazo, nalangiza poimbira cholemekeza. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nati, Chiwembu, chiwembu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayangʼana, ndipo anaona mfumu itayima pa chipilala chake chapakhomo. Atsogoleri ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderali amakondwerera ndi kuyimba malipenga ndiponso oyimba ndi zida amatsogolera matamando. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake ndipo anafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yace polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m'dziko anakondwera, naomba amalipenga; oyimbira omwe analiko ndi zoyimbirazo, nalangiza poyimbira colemekeza. Pamenepo Ataliya anang'amba zobvala zace, nati, Ciwembu, ciwembu.