2 Chronicles 23:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wansembe Yehoyada adabwera nawo atsogoleri a gulu lankhondo aja naŵauza kuti, “Mtulutseni ameneyu pakati pa mizere mwandandayo. Ndipo aliyense amene amtsate, mumuphe ndi lupanga.” Wansembeyo adaanenadi kuti, “Musamphere m'Nyumba ya Chauta ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehoyada wansembe anatuluka nao atsogoleri a mazana akuyang'anira khamu la nkhondo, nanena nao, Mtulutseni mkaziyo pakati pa mipambo; ndipo aliyense womtsata aphedwe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Msamphere m'nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe Yehoyada anatumiza olamulira magulu a anthu 100 aja, amene amayangʼanira asilikali ndipo anawawuza kuti, “Mutulutseni ameneyu pakati pa mizere yanu ndipo muphe aliyense amene adzamutsata.” Pakuti ansembe anati, “Musamuphere mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova,”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehoyada wansembe anaturuka nao atsogoleri a mazana akuyang'anira khamu la nkhondo, nanena nao, Mturutseni mkaziyo pakati pa mipambo; ndipo ali yense womtsata aphedwe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Msamphere m'nyumba ya Yehova.