2 Chronicles 23:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho anthu onsewo adapita ku nyumba ya Baala, nakaigwetsa. Maguwa ake ndi mafano ake adaŵaphwanyaphwanya. Kenaka anthuwo adaphanso Matani, wansembe wa Baala, patsogolo pa maguwawo pomwepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi anthu onse anamuka kunyumba ya Baala, naipasula, naphwanya maguwa ake a nsembe, ndi mafano ake; namupha Matani wansembe wa Baala kumaguwa a nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse anapita ku kachisi wa Baala ndipo anamugwetsa. Iwo anaphwanya maguwa ndi mafano ndi kupha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi anthu onse anamuka ku nyumba ya Baala, naipasula, naphwanya maguwa ace a nsembe, ndi mafano ace; namupha Matana wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe.