2 Chronicles 23:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehoyada adaika ansembe a fuko la Levi kuti azilonda Nyumba ya Chauta. Paja Aleviwo Davide adaaŵaika kuti aziyang'anira Nyumba ya Chauta, ndi kumapereka nsembe zopsereza kwa Chauta, monga zidalembedwa m'malamulo a Mose kuti azipereka akukondwa ndipo akumaimba, potsata lamulo la Davide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehoyada anaika mayang'aniro a nyumba ya Yehova m'dzanja la ansembe Aleviwo, amene Davide anawagawa, ayang'anire nyumba ya Yehova; napereka nsembe zopsereza za Yehova monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose, ndi kukondwera ndi kuimbira, monga mwa chilangizo cha Davide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehoyada anayika ansembe, omwe anali Alevi kukhala oyangʼanira Nyumba ya Yehova, amene Davide anawapatsa ntchito yoti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova mʼNyumba ya Mulungu, monga zinalembedwa mʼmalamulo a Mose kuti azitero akukondwera ndi kuyimba monga Davide analamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehoyada anaika mayang'aniro a nyumba ya Yehova m'dzanja la ansembe Aleviwo, amene Davide anawagawa, ayang'anire nyumba ya Yehova; napereka nsembe zopsereza za Yehova monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose, ndi kukondwera ndi kuyimbira, monga mwa cilangizo ca Davide.