2 Chronicles 23:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adandanditsa atsogoleri, nduna, akazembe a anthu ndi anthu onse am'dzikomo. Onsewo adaperekeza mfumu kuchokera ku Nyumba ya Chauta, nakalowa m'nyumba ya mfumu podzera pa khomo lake lapamwamba; ndipo kumeneko adaikhazika mfumuyo pa mpando waufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natenga atsogoleri a mazana, ndi omveka, ndi akazembe a anthu, ndi anthu onse a m'dziko, natsika ndi mfumu kunyumba ya Yehova; nalowera pa chipata cha kumtunda m'nyumba ya mfumu, namkhalitsa mfumu pa mpando wa ufumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anatenga olamulira magulu a anthu 100, anthu otchuka, olamulira anthu ndi anthu onse a mʼderalo ndipo anabweretsa mfumu kuchokera ku Nyumba ya Mulungu. Iwo anapita ku nyumba yaufumu kudzera ku Chipata Chakumitu ndipo anayikira mfumu mpando wolemekezeka,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natenga atsogoleri a mazana, ndi omveka, ndi akazembe a anthu, ndi anthu onse a m'dziko, natsika ndi mfumu ku nyumba ya Yehova; nalowera pa cipata ca kumtunda m'nyumba ya mfumu, namkhalitsa mfumu pa mpando wa ufumu.