2 Chronicles 23:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musalole aliyense kuti aloŵe m'Nyumba ya Chauta, koma ansembe ndi Alevi okha amene amatumikira. Iwo angathe kuloŵa poti ngoyeretsedwa. Anthu onse azimvera lamulo la Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma asalowe mmodzi m'nyumba ya Yehova, ansembe okha, ndi Alevi otumikira, alowe iwowa; pakuti ndiwo opatulika; koma anthu onse asunge udikiro wa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musalole aliyense kulowa mʼNyumba ya Yehova kupatula ansembe ndi Alevi amene akutumikira. Iwo atha kutero chifukwa apatulidwa koma anthu ena onse ayenera kumvera zimene Yehova walamula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma asalowe mmodzi m'nyumba ya Yehova, ansembe okha, ndi Alevi otumikira, alowe iwowa; pakuti ndiwo opatulika; koma anthu onse asunge udikiro wa Yehova.