2 Chronicles 23:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Alevi ndi anthu onse a ku Yuda adachitadi zonse monga m'mene wansembe Yehoyada adaŵalamulira. Aliyense adabwera ndi anthu ake amene ankadzayamba ntchito yao yotumikira pa sabata, pamodzinso ndi anthu amene ankasiya ntchito yao yotumikira pa sabata. Pakuti wansembe Yehoyada sadaŵaloleze kuchokapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo Alevi ndi Ayuda onse anachita monga mwa zonse anawauza Yehoyada wansembe; natenga yense amuna ake alowe tsiku la Sabata pamodzi ndi otuluka tsiku la Sabata; pakuti Yehoyada wansembe sanamasule zigawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alevi ndi anthu onse a ku Yuda anachita monga momwe wansembe Yehoyada anawalamulira. Aliyense anatenga anthu ake amene ankagwira ntchito pa Sabata ndi amene amapita kukapuma, pakuti wansembe Yehoyada sanalole gulu lililonse kuti lipite.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo Alevi ndi Ayuda onse anacita monga mwa zonse anawauza Yehoyada wansembe; natenga yense amuna ace alowe dzuwa la Sabata pamodzi ndi oturuka dzuwa la Sabata; pakuti Yehoyada wansembe sanamasula zigawo.