2 Chronicles 23:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehoyadayo adapatsa atsogoleri aja mikondo ndi zishango zazikulu ndi zazing'ono, zimene zidaali za mfumu Davide. Zimenezi zinkasungidwa mu Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Yehoyada wansembe anapereka kwa akazembe a mazana mikondo, ndi zikopa, ndi malaya achitsulo, zinali za mfumu Davide, zokhala m'nyumba ya Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehoyada anapereka kwa atsogoleri a magulu a anthu 100 mikondo ndi zishango zazikulu ndi zazingʼono zimene zinali za Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Yehoyada wansembe anapereka kwa akazembe a mazana mikondo, ndi zikopa, ndi maraya acitsulo, zinali za mfumu Davide, zokhala m'nyumba, ya Mulungu.