2 Chronicles 24:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene adalembedwawo ankagwiradi ntchito, ndipo ntchito yokonzayo idapita m'tsogolo akuigwira ndi manja ao. Choncho anthuwo Nyumba ya Chauta ija adaisandutsanso monga momwe idaaliri kale, ndipo adailimbitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo anachita ogwira ntchito, nikula ntchito mwa dzanja lao, nakhazikitsa iwo nyumba ya Mulungu monga mwa maonekedwe ake, nailimbitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amene ankagwira ntchito anali odziwa bwino, ndipo ntchitoyo inagwiridwa bwino ndi manja awo. Iwo anamanganso Nyumba ya Mulungu motsatira mapangidwe ake oyamba ndipo anayilimbitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo anacita ogwira nchito, nikula nchito mwa dzanja lao, nakhazikitsa iwo nyumba ya Mulungu monga mwa maonekedwe ace, nailimbitsa.