2 Chronicles 24:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ataimaliza, ndalama zotsala adabwera nazo kwa mfumu ndi kwa Yehoyada. Iwo adapanga ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta ndi ndalamazo, ziŵiya zogwirira ntchito ndiponso za nsembe zopsereza. Adapanganso mbale za lubani ndiponso ziŵiya zagolide ndi zasiliva. Anthu ankapereka nsembe zopsereza ku Nyumba ya Chauta kosalekeza, pa nthaŵi yonse ya Yehoyada.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golide ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamaliza, iwo anabweretsa ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, ndipo anazigwiritsira ntchito popangira zida za mʼNyumba ya Yehova: ziwiya zogwiritsa ntchito potumikira ndi popereka nsembe zopsereza, komanso mbale ndi ziwiya zagolide ndi siliva. Nthawi yonse ya moyo wa Yehoyada, nsembe zopsereza zinkaperekedwa mosalekeza mʼNyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golidi ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.