2 Chronicles 24:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu adasiya Nyumba ya Chauta, Mulungu wa makolo ao, namatumikira mafano. Tsono mkwiyo wa Mulungu udagwera anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu, chifukwa cha tchimo laoli.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo ao, natumikira zifanizo, ndi mafano; ndipo mkwiyo unawagwera Yuda ndi Yerusalemu, chifukwa cha kupalamula kwao kumene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anasiya Nyumba ya Yehova, Mulungu wa makolo awo ndipo anapembedza Asera ndi mafano. Chifukwa cha kulakwa kwawo, mkwiyo wa Yehova unabwera pa Yuda ndi Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo ao, natumikira zifanizo, ndi mafano; ndipo mkwiyo unawagwera Yuda ndi Yerusalemu, cifukwa ca kuparamula kwao kumene.