2 Chronicles 24:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mzimu wa Mulungu udaloŵa mwa Zekariya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye adaimirira pakati pa anthu naŵauza kuti, “Chauta akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukuchimwira malamulo a Chauta? Ndithu simudzapindula kanthu?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mzimu wa Mulungu unavala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mzimu wa Mulungu unabwera pa Zekariya mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anayimirira pamaso pa anthu ndipo anati, “Zimene Mulungu akunena ndi Izi: ‘Chifukwa chiyani simukumvera Malamulo a Yehova? Simudzapindula. Chifukwa mwasiya Yehova, Iyenso wakusiyani.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mzimu wa Mulungu unabvala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.