2 Chronicles 24:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa kutha kwa chaka, gulu lankhondo la ku Siriya lidadzamenyana ndi Yowasi. Adabwera ku Yuda ndi ku Yerusalemu, napha akazembe onse a anthu pakati pa anthuwo. Ndipo adatumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika, podzanso nyengoyi khamu la nkhondo la Aaramu linamkwerera, nafika iwo ku Yuda ndi Yerusalemu, naononga mwa anthu akalonga onse a anthu, natumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakutha kwa chaka, gulu lankhondo la Aramu linadzamenyana ndi Yowasi. Linalowa mu Yuda ndi mu Yerusalemu ndi kupha atsogoleri onse a anthu. Zonse zimene analanda anazitumiza kwa mfumu ya ku Damasiko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika, podzanso nyengoyi khamu la nkhondo la Aaramu linamkwerera, nafika iwo ku Yuda ndi Yerusalemu, naononga mwa anthu akalonga onse a anthu, natumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko.