2 Chronicles 24:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asiriya aja atamsiya wovulazidwa kwambiri, anyamata ake adamchita chiwembu, chifukwa cha magazi a mwana wa Yehoyada wansembe uja, ndipo adamphera pabedi pake. Motero iyeyo adafa. Ndipo adamuika m'manda mu mzinda wa Davide, koma sadamuike m'manda a mafumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atamchokera (popeza anamsiya wodwala nthenda zazikulu), anyamata ake anamchitira chiwembu, chifukwa cha mwazi wa ana a Yehoyada wansembe, namupha pakama pake, namwalira iye; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma osamuika m'manda a mafumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Aaramu amachoka, anasiya Yowasi atavulazidwa kwambiri. Akuluakulu ake anamuchitira chiwembu chifukwa anapha mwana wa wansembe Yehoyada, ndipo anamupha ali pa bedi pake. Choncho anafa ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide, koma osati manda a mafumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atamcokera (popeza anamsiya wodwala nthenda zazikuru), anyamata ace anamcitira ciwembu, cifukwa ca mwazi wa ana a Yehoyada wansembe, namupha pakama pace, namwalira iye; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma osamuika m'manda a mafumu.