2 Chronicles 24:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, naŵauza kuti, “Pitani ku mizinda ya Yuda, mukasonkhetse ndalama pakati pa Aisraele onse, kuti muzikonzera Nyumba ya Chauta wanu chaka ndi chaka. Muwone kuti zimenezi zichitike mwachangu.” Koma Alevi sadachite zimenezo mofulumira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, nanena nao, Mutuluke kunka kumidzi ya Yuda, ndi kusonkhanitsa kwa Aisraele onse ndalama zakukonzetsa nyumba ya Mulungu wanu chaka ndi chaka; ndipo inu fulumirani nayo ntchitoyi. Koma Alevi sanafulumire nayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayitanitsa pamodzi ansembe ndi Alevi ndipo anawawuza kuti, “Pitani ku mizinda ya Yuda ndi kukasonkhetsa ndalama za pa chaka kwa Aisraeli onse zokonzera Nyumba ya Mulungu wanu. Chitani zimenezi tsopano.” Koma Alevi sanachite zimenezi mwachangu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, nanena nao, Muturuke kumka ku midzi ya Yuda, ndi kusonkhanitsa kwa Aisrayeli onse ndarama zakukonzetsa nyumba ya Mulungu wanu caka ndi caka; ndipo inu fulumirani nayo nchitoyi. Koma Alevi sanafulumira nayo.