2 Chronicles 24:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero mfumu idaitana Yehoyada mkulu wa ansembe nimfunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani sudaŵauze Alevi kuti asonkhetse ndalama ku Yuda ndi ku Yerusalemu, ndalama zimene adalamula Mose mtumiki wa Chauta ku mpingo wonse wa Aisraele, ndalama zokonzera hema lamsonkhano?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkulu wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kuchokera m'Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israele, ukhale wa chihema cha umboni?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mfumu inayitanitsa Yehoyada, mkulu wa ansembe ndipo inati kwa iye, “Kodi nʼchifukwa chiyani simunawuze Alevi kuti asonkhetse ndalama ku Yuda ndi Yerusalemu, msonkho umene anakhazikitsa Mose mtumiki wa Yehova ndiponso gulu lonse la Aisraeli mu tenti yaumboni?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkuru wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kucokera m'Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israyeli, ukhale wa cihema ca umboni?