2 Chronicles 25:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amaziya anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 29 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yehowadani wa ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amaziya anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la make ndiye Yehowadani wa ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amaziya anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 29. Dzina la amayi ake linali Yehoyadini wa ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amaziya anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la mace ndiye Yehoadana wa ku Yerusalemu.