2 Chronicles 25:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Amaziya adalichotsa gulu lankhondo la ku Efuremu kuti libwerere kwao. Gulu lankhondolo lidaŵapsera mtima kwambiri anthu a ku Yudawo, ndipo lidapita kwao lili lokwiya kwabasi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Amaziya anawapambutsa, ndiwo ankhondo anamdzera kuchokera ku Efuremu, amuke kwao; potero adapsa mtima kwambiri pa Yuda, nabwera kwao ndi kutentha mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Amaziya anachotsa asilikali amene anabwera kwa iye kuchokera ku Efereimu ndipo anawatumiza kwawo. Iwo anakwiyira anthu a ku Yuda ndipo anapita kwawo atapsa mtima kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Amaziya anawapambutsa, ndiwo ankhondo anamdzera kucokera ku Efraimu, amuke kwao; potero adapsa mtima kwambiri pa Yuda, nabwera kwao ndi kutentha mtima.