2 Chronicles 25:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Yuda adagwira anthu ena amoyo okwaniranso 10,000. Adakwera nawo pamwamba pa thanthwe, naŵaponya pansi kuchoka pamenepo. Ndiye onsewo adangotekedzeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ana a Yuda anagwira zikwi khumi ena amoyo, nabwera nao pamwamba pa thanthwe, naphwanyika onsewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gulu la ankhondo la Yuda linagwiranso anthu amoyo 10,000, napita nawo pamwamba pa thanthwe ndipo anawaponya pansi kotero kuti onse ananyenyeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ana a Yuda anagwira zikwi khumi ena amoyo, nabwera nao pamwamba pa thanthwe, nawakankha pamwamba pa thanthwe, naphwanyika onsewo.