2 Chronicles 25:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma gulu lankhondo limene Amaziya adalibweza lija, osalilola kuti lipite nao ku nkhondo, lidakathira nkhondo mizinda ya Yuda kuyambira ku Samariya mpaka ku Betehoroni, naphako anthu okwanira 3,000 ku mizindayo, ndipo adatengako zofunkha zambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma amuna a nkhondo amene Amaziya anawabwereretsa, kuti asamuke naye kunkhondo, anagwera midzi ya Yuda kuyambira Samariya kufikira Betehoroni, nakantha a iwowa zikwi zitatu, nalanda zofunkha zambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyi asilikali amene Amaziya anawabweza ndipo sanawalole kuti achite nawo nkhondo, anakathira nkhondo mizinda ya Yuda kuyambira ku Samariya mpaka ku Beti-Horoni. Iwo anapha anthu 3,000 ndipo anafunkha katundu wambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma amuna a nkhondo amene Amaziya anawabwereretsa, kuti asamuke naye kunkhondo, anagwera midzi ya Yuda kuyambira Samariya kufikira Betihoroni, nakantha a iwowa zikwi zitatu, nalanda zofunkha zambiri.