2 Chronicles 25:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Amaziya atabwerako kuja adakapha Aedomuku, adabwera ndi milungu ya anthu a ku Seiri, naiika kuti ikhale milungu yake. Ndipo ankaipembedza ndi kumaifukizira lubani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, atafika Amaziya atatha kuwapha Aedomu, ndi kubwera nayo milungu ya ana a Seiri, anaiika ikhale milungu yake, naigwadira, naifukizira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amaziya atabwerera kuja anakapha Aedomu, anabweretsa milungu ya anthu a ku Seiri. Ndipo anayika kuti ikhale milungu yake, ankayipembedza ndi kupereka nsembe zopsereza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, atafika Amaziya atatha kuwapha Aedomu, ndi kubwera nayo milungu ya ana a Seiri, anaiika ikhale milungu yace, naigwadira, naifukizira,