2 Chronicles 25:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta adamkwiyira Amaziya. Adatuma mneneri kwa iyeyo, kukamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukufuna milungu ya anthu, imene sidathe kuŵapulumutsa anthuwo m'manja mwanu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Amaziya, ndipo anamtumira mneneri amene anati, Mwafuniranji milungu ya anthu imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja lanu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anakwiyira Amaziya, ndipo anamutumizira mneneri amene anati, “Nʼchifukwa chiyani mukupembedza milungu ya anthu awa, imene sinathe kupulumutsa anthu ake mʼdzanja lanu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mkwiyo wa Mulungu unayakira Amaziya, ndipo anamtumira mneneri amene anati, Mwafuniranji milungu ya anthu imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja lanu?