2 Chronicles 25:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene mneneriyo ankalankhula, mfumu ija idamufunsa kuti, “Kodi iweyo tidakuika kuti ukhale phungu wa mfumu? Khala chete! Ufuna kuphedweranji?” Mneneriyo adakhala chete kanthaŵi, kenaka adati, “Ndikudziŵa kuti Mulungu watsimikiza zoti akuwonongeni inu, chifukwa chakuti inuyo mwachita zimenezi osamvera uphungu wanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ali kuyankhula, mfumu inati, “Kodi ife takusankha iwe kuti ukhale mlangizi wa mfumu? Khala chete! Ufuna kuphedweranji?” Choncho mneneriyo analeka koma anati, “Ine ndikudziwa kuti Mulungu watsimikiza kukuwonongani chifukwa mwachita izi ndipo simunamvere uphungu wanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwacita ici ndi kusamvera kupangira kwanga.