2 Chronicles 25:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ina Amaziya, mfumu ya ku Yuda, adachita upo. Adatumiza mau kwa Yehowasi, mwana wa Yehowahazi, mwana wa Yehu, mfumu ya ku Israele, mau omuputa akuti, “Ubwere kuno, udzachione.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Amaziya mfumu ya Yuda anafunsana ndi ompangira, natumiza kwa Yowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani, tionane maso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amaziya mfumu ya ku Yuda, atafunsa alangizi ake, anatumiza mawu awa kwa Yowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu, mfumu ya Israeli: “Bwera udzakumane nane maso ndi maso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Amaziya mfumu ya Yuda anafunsana ndi ompangira, natumiza kwa Yoasi mwana wa Yehoahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Idzani, tionane maso.