2 Chronicles 25:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adabweza mau kwa Amaziya, mfumu ya ku Yuda, kuti “Padangotere, mtungwi wa ku Lebanoni udatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni kuti, ‘Pereka mwana wako wamkazi kwa mwana wanga kuti amkwatire.’ Koma chilombo cha ku Lebanoni chidadzera pamenepo nkuupondereza mtungwiwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Yowasi mfumu ya Israele anatumiza kwa Amaziya mfumu ya Yuda ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; koma nyama ya kuthengo ya ku Lebanoni inapitapo, nipondereza mtungwi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yowasi mfumu ya Israeli inayankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti, “Nthawi ina kamtengo kaminga ka ku Lebanoni kanatumiza mawu kwa mkungudza wa ku Lebanoni kuti, ‘Pereka mwana wako wamkazi kwa mwana wanga kuti amukwatire!’ Koma chirombo cha ku Lebanoni chinabwera ndi kupondaponda mtengo wa minga uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Yoasi mfumu ya Israyeli anatumiza kwa Amaziya mfumu ya Yuda ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebano unatumiza kwa mkungudza wa ku Lebano, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wace; koma nyama ya kuthengo ya ku Lebano inapitapo, nipondereza mtungwi.