2 Chronicles 25:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inde, iwe ukuti wagonjetsa Edomu, ndipo tsopano ukudzikuza nkumadzitamira kupambana kwakoko. Koma ai tsono, khala kwanu komweko. Bwanji ukufuna kuutsa mavuto dala? Bwinotu, ungagwe, iweyo pamodzi ndi anthu a ku Yuda!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukuti, Taonani, ndakantha Aedomu, nukwezeka mtima wanu kudzikuza; khalani kwanu tsopano, mungadziutsire tsoka, mungagwe, inu, ndi Yuda pamodzi ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe ukuti wagonjetsa Edomu, ndipo tsopano ukudzikuza ndi kudzitamandira, koma khala kwanu komweko! Nʼchifukwa chiyani ukufuna mavuto ndi kudzichititsa kuti ugwe pamodzinso ndi Yuda?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukuti, Taonani, ndakantha Aedomu, nukwezeka mtima wanu kudzikuza; khalani kwanu tsopano, mungadziutsire tsoka, mungagwe, inu, ndi Yuda pamodzi ndi inu.