2 Chronicles 25:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Amaziya sadasamaleko zimenezi, pakuti ndi Mulungu yemwe adaafuna kuti aŵapereke anthuwo m'manja mwa adani ao, chifukwa chakuti iwowo ankapembedza milungu ya Aedomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma wosamvera Amaziya, pakuti ncha Mulungu ichi kuti awapereke m'dzanja la adani ao; popeza anafuna milungu ya Edomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe Amaziya sanamvere pakuti ndi Mulungu amene anakonzeratu kuti awapereke kwa Yehowasi, chifukwa iwo amapembedza milungu ya ku Edomu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma wosamvera Amaziya, pakuti nca Mulungu ici kuti awapereke m'dzanja la adani ao; popeza anafuna milungu ya Edomu.