2 Chronicles 25:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ku Betesemesiko Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adagwirako Amaziya mfumu ya ku Yuda, mwana wa Yowasi, mdzukulu wa Ahaziya, nabwera naye ku Yerusalemu. Ndipo Yehowasi adagumula khoma la Yerusalemu mamita 200, kuyambira ku chipata cha Efuremu mpaka ku chipata Chapangodya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Yehowahazi, ku Betesemesi, nabwera naye ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira chipata cha Efuremu kufikira chipata cha kungodya, mikono mazana anai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehowahazi mfumu ya Israeli inagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi, mwana wa Ahaziya ku Beti-Semesi. Yehowasi anabwera naye ku Yerusalemu ndipo anagwetsa khoma la Yerusalemu kuyambira pa Chipata cha Efereimu mpaka ku Chipata Chapangodya, khoma lotalika mamita 180.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoasi mfumu ya Israyeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yoasi mwana wa Yehoahazi, ku Betisemesi, nabwera naye ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira cipata ca Efraimu kufikira cipata ca kungondya, mikono mazana anai.