2 Chronicles 25:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo adalanda golide ndi siliva yense ndi ziŵiya zonse zimene adazipeza m'Nyumba ya Chauta zosungidwa ndi Obededomu. Adatenganso chuma cha ku nyumba ya mfumu, nkugwira anthu ena ngati chikole, nabwerera ku Samariya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natenga golide ndi siliva zonse, ndi zipangizo zonse zopezeka m'nyumba ya Mulungu kwa Obededomu, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwerera kunka ku Samariya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anatenga golide ndi siliva yense ndi zida zonse zimene zimapezeka mʼNyumba ya Mulungu zimene ankazisamalira Obedi-Edomu, pamodzinso ndi chuma cha mʼnyumba yaufumu ndipo anatenga anthu ngati chikole.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natenga golidi ndi siliva zonse, ndi zipangizo zonse zopezeka m'nyumba ya Mulungu kwa Obedi Edomu, ndi cuma ca nyumba ya mfumu, acikole omwe; nabwerera kumka ku Samariya.