2 Chronicles 25:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuyambira nthaŵi imene iye adafulatira Chauta, anthu adamchita chiwembu ku Yerusalemu, iyeyo nkuthaŵira ku Lakisi. Koma adaniwo adatuma anzao kuti amlondole ku Lakisiko, ndipo adakamphera komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chipatukire Amaziya kusatsata Yehova, namchitira chiwembu m'Yerusalemu, nathawira ku Lakisi iyeyu; koma anatuma omtsatira ku Lakisi, namupha komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyambira nthawi imene Amaziya analeka kutsatira Yehova anthu anamukonzera chiwembu mu Yerusalemu ndipo anathawira ku Lakisi, koma adaniwo anatumiza anthu ku Lakisiko ndipo anamupha komweko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cipambukire Amaziya kusatsata Yehova, anamcitira ciwembu m'Yerusalemu, nathawira ku Lakisi iyeyu; koma anatuma omtsatira ku Lakisi, namupha komweko.