2 Chronicles 25:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ana ao sadaŵaphe, potsata zimene zidalembedwa m'malamulo a m'buku la Mose, m'mene Chauta adalamula kuti, “Atate sadzaphedwa chifukwa cha ana ao, kapena ana kuphedwa chifukwa cha atate ao. Koma munthu aliyense adzafera machimo ake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma sanaphe ana ao, koma anachita monga umo mulembedwa m'chilamulo, m'buku la Mose, monga Yehova analamulira, ndi kuti, Atate asafere ana, ndi ana asafere atate; koma yense afere tchimo lakelake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe iye sanaphe ana awo koma anatsatira zolembedwa mʼbuku la Mose, mʼmene Yehova analamula kuti, “Makolo sadzaphedwa chifukwa cha ana awo kapena ana kuphedwa chifukwa cha makolo awo. Aliyense adzafera machimo ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma sanapha ana ao, koma anacita monga umo mulembedwa m'cilamulo, m'buku la Mose, monga Yehova analamulira, ndi kuti, Atate asafere ana, ndi ana asafere atate; koma yense afere chimo lace lace.