2 Chronicles 25:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Amaziya adasonkhanitsa Ayuda naŵakhazika potsata mabanja ao. Adaŵapatsanso atsogoleri a anthu zikwi ndi a anthu mazana, ku Yuda konse ndi ku Benjamini komwe. Adasonkhanitsa anthu a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo. Anthuwo analipo 300,000, anthu osankhika, okhoza nkhondo, odziŵa kugwira mkondo ndi chishango.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Amaziya anamemeza Ayuda, nawaika monga mwa nyumba za atate ao, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo onse a Yuda ndi Benjamini; nawawerenga a zaka makumi awiri ndi mphambu, nawapeza amuna osankhika zikwi mazana atatu akutulukira kunkhondo, ogwira mkondo ndi chikopa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amaziya anasonkhanitsa anthu a ku Yuda ndipo anawapatsa zochita molingana ndi mabanja awo kukhala anthu olamulira 1,000, ndi olamulira 100 pa Ayuda onse ndi Benjamini. Ndipo iye anawerenga amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo napeza kuti analipo amuna 300,000 okonzeka kugwira ntchito ya usilikali, okhoza kugwiritsa ntchito mkondo ndi chishango.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Amaziya anamemeza Ayuda, nawaika monga mwa nyumba za atate ao, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo onse a Yuda ndi Benjamini; nawawerenga a zaka makumi awiri ndi mphambu, nawapeza amuna osankhika zikwi mazana atatu akuturukira kunkhondo, ogwira mkondo ndi cikopa.