2 Chronicles 25:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthu wina wa Mulungu adadza kwa iye, namuuza kuti, “Inu amfumu, musapite ndi gulu lankhondo la ku Israele, pakuti Chauta sali nawo anthu ku Israele, ana a Efuremuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anamdzera munthu wa Mulungu, kuti, Mfumu, khamu la nkhondo la Israele lisapite nanu; pakuti Yehova sakhala ndi Israele, sakhala ndi ana onse a Efuremu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma munthu wa Mulungu anabwera kwa iye ndipo anati, “Inu mfumu, asilikali awa ochokera ku Israeli asapite ndi inu, pakuti Yehova sali ndi Israeli kapena ndi aliyense wa anthu a Efereimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anamdzera munthu wa Mulungu, kuti, Mfumu, khamu la nkhondo la Israyeli lisapite nanu; pakuti Yehova sakhala ndi Israyeli, sakhala ndi ana onse a Efraimu.