2 Chronicles 25:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukaganiza kuti mudzakhala ndi mphamvu kunkhondoko mwa njira imeneyi, Mulungu adzakugonjetsani pamaso pa adani. Pakuti Mulungu ndiye ali ndi mphamvu za kuthandiza ndi za kugonjetsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati mumuka, chitani, limbikani kunkhondo, Mulungu adzakugwetsani pamaso pa adani; pakuti Mulungu ali nayo mphamvu yakuthandiza ndi yakugwetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale mupite ndi kuchita nkhondo molimba mtima, Mulungu adzakugonjetsani pamaso pa adani anu, pakuti Mulungu ali ndi mphamvu yothandiza kapena kugonjetsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati mumuka, citani, limbikani kunkhondo, Mulungu adzakugwetsani pamaso pa adani; pakuti Mulungu ali nayo mphamvu yakuthandiza ndi yakugwetsa.