2 Chronicles 25:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amaziya adafunsa munthu wa Mulungu uja kuti, “Koma nanga bwanji za makilogramu a siliva aja amene ndapatsa gulu lankhondo la ku Israele?” Munthu wa Mulunguyo adayankha kuti, “Chauta angathe kukupatsani zambiri kupambana zimenezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Amaziya anati kwa munthu wa Mulungu, Koma nanga titani nao matalente zana limodzi ndinapatsa ankhondo a Israele? Nati munthu wa Mulungu, Yehova ali nazo zoposa izi kukupatsani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amaziya anafunsa munthu wa Mulungu kuti, “Koma nanga za makilogalamu aja a siliva amene ndapereka kwa asilikali a Israeli?” Munthu wa Mulungu anayankha kuti, “Yehova atha kukupatsani zambiri kuposa zimenezo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Amaziya anati kwa munthu wa Mulungu, Koma nanga titani nao matalente zana limodzi ndinapatsa ankhondo a Israyeli? Nati munthu wa Mulungu, Yehova ali nazo zoposa izi kukupatsani.