2 Chronicles 26:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adamanga nsanja ku chipululu ndi kukumba zitsime zambiri, poti anali ndi ziŵeto zambiri ku madambo ndi ku zigwa. Analinso ndi anthu olima minda ndi anthu omasamala mphesa ku mapiri, ndiponso ku maiko achonde, poti ankakonda kulima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namanga nsanja m'chipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi kunthaka yopatsa bwino; pakuti anakonda kulima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anamanganso nsanja ku chipululu ndi kukumbanso zitsime zambiri chifukwa anali ndi ziweto zambiri mʼmbali mwa phiri ndi ku zigwa. Iye anali ndi anthu amene ankagwira ntchito mʼminda yake ndiponso mʼminda yake ya mphesa mʼphiri ndi malo achonde, pakuti ankakonda nthaka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namanga nsanja m'cipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi ku nthaka yopatsa bwino; pakuti ndiye mlimi.