2 Chronicles 26:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komanso Uziyayo anali ndi gulu la asilikali odziŵa nkhondo. Anali m'magulumagulu potsata dongosolo limene adaalikonza mlembi Yeiyele ndi Maaseiya, mkulu wankhondo. Amene ankaŵalamulira asilikaliwo anali Hananiya, mmodzi mwa nduna za mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uziya anali nalonso khamu la anthu a nkhondo, otuluka kunkhondo magulu; nawawerenga monga mwa mawerengedwe ao ndi dzanja la mlembi Yeiyele, ndi kapitao Maaseiya, monga anawauza Hananiya kazembe wina wa mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uziya anali ndi gulu lankhondo lophunzitsidwa bwino, lokonzekera kupita ku nkhondo mʼmagulu monga mwa chiwerengero chawo chimene mlembi Yeiyeli ndi Maaseya anasonkhanitsa motsogozedwa ndi Hananiya mmodzi mwa akuluakulu a mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uziya anali nalonso khamu la anthu a nkhondo, oturuka kunkhondo magulu; nawawerenga monga mwa mawerengedwe ao ndi dzanja la mlembi Yeyeli, ndi kapitao Maseya, monga anawauza Hananiya kazembe wina wa mfumu.