2 Chronicles 26:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri ameneŵa ankalamulira gulu lankhondo lokwanira asilikali 307,500, amene ankatha kumenya nkhondo mwamphamvu, kuthandiza mfumu polimbana ndi adani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'dzanja mwao munali khamu la nkhondo zikwi mazana atatu mphambu zikwi zisanu ndi ziwiri kudza mazana asanu ochita nkhondo ndi mphamvu yaikulu, kuthandiza mfumu alimbane ndi adani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pansi pa ulamuliro wawo panali asilikali 307,500 ophunzitsidwa nkhondo, gulu lamphamvu lothandiza mfumu kulimbana ndi adani ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'dzanja mwao munali khamu la nkhondo zikwi mazana atatu mphambu zikwi zisanu ndi ziwiri kudza mazana asanu ocita nkhondo ndi mphamvu yaikuru, kuthandiza mfumu alimbane ndi adani.