2 Chronicles 26:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku Yerusalemu anthu aluso adapanga makina amene ankaŵakweza pa nsanja ndi pa malo onse andonyo, kuti anthu aziponyera mivi ndiponso miyala ikuluikulu. Choncho mbiri ya Uziya idamveka nikafika kutali, chifukwa anali atathandizidwa kodabwitsa, mpaka adakhala wamphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Napanga m'Yerusalemu makina, opangidwa ndi eni luso, akhale pansanja ndi kungodya, aponye nao mivi ndi miyala yaikulu. Ndi dzina lake linamveka kutali; pakuti anathandizidwa modabwitsa, mpaka analimbikatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mu Yerusalemu anapanga makina okonzedwa ndi anthu aluso amene amagwiritsidwa ntchito pa malo otetezera a pa nsanja ndi pa ngodya kuponyera mivi ndi kugubuduzira miyala. Mbiri yake inamveka kutali ndi ponseponse pakuti anathandizidwa kwambiri mpaka anakhala wamphamvu kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Napanga m'Yerusalemu makina, opangidwa ndi eni luso, akhale pansanja ndi kungondya, aponye nao mibvi ndi miyala yaikuru. Ndi dzina lace linamveka kutali; pakuti anathandizidwa modabwiza, mpaka analimbikatu.