2 Chronicles 26:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Uziyayo mphamvu zake zitachuluka, adayamba kunyada ndipo kunyada kwakeko kudamuwonongetsa. Anali wosakhulupirika kwa Chauta Mulungu wake, ndipo adaloŵa ku Nyumba ya Chauta kuti akafukize lubani pa guwa lofukizapo lubani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma atakhala wamphamvu, mtima wake unakwezeka momuononga, nalakwira Yehova Mulungu wake; popeza analowa m'Kachisi wa Yehova kufukiza pa guwa la nsembe la chofukiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene Uziya anakhala wamphamvu kwambiri, kunyada kwake kunamuwononga. Iye sanakhulupirike kwa Yehova Mulungu wake, ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova kukafukiza lubani pa guwa lofukizira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma atakhala wamphamvu, mtima wace unakwezeka momuononga, nalakwira Yehova Mulungu wace; popeza analowa m'Kacisi wa Yehova kufukiza pa guwa la nsembe la cofukiza.