2 Chronicles 26:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ansembewo adamletsa mfumu Uziya namuuza kuti, “Pepani, mfumu Uziya, sindinu amene muyenera kufukiza lubani kwa Chauta, koma ansembe, ana a Aaroni, amene adaŵapatula kuti azifukiza lubani. Chokaniko ku malo opatulika kwambiriŵa. Kutereku mwalakwa, ndipo ulemerero wa Chauta wakuchokerani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
natsutsana ndi mfumu Uziya, nati kwa iye, Sikuyenera inu, Uziya, kufukizira Yehova koma ansembe, ana a Aroni opatulidwira kufukiza; tulukani m'malo opatulika; pakuti mwalakwa; Yehova Mulungu sakulemekezanipo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anatsutsana naye ndipo anati, “Sibwino kuti inu mfumu muzifukiza lubani koma zidzukulu za Aaroni, zimene zinapatulidwa kuti zizifukiza lubani. Chokani pa malo opatulika ano, pakuti inu mwakhala osakhulupirika, ndipo simudzalemekezedwa ndi Yehova Mulungu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
natsutsana ndi mfumu Uziya, nati kwa iye, Sikuyenera inu, Uziya, kufukizira Yehova, koma ansembe, ana a Aroni opatulidwira kufukiza; turukani m'malo opatulika; pakuti mwalakwa; Yehova Mulungu sakulemekezanipo.