2 Chronicles 26:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Uziya adapsa mtima. Tsono m'manja mwake munali chofukizira lubani. Ndipo atakwiyira ansembewo, khate lidatuluka pamphumi pake, ansembe aja akuwona, m'Nyumba ya Chauta, pafupi ndi guwa lofukizirapo lubani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Uziya anapsa mtima, mbale ya zofukiza ili m'dzanja lake kufukiza nayo; ndipo pakupsa mtima nao ansembe, khate linabuka pamphumi pake, pamaso pa ansembe m'nyumba ya Yehova, pambali pa guwa lofukizapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uziya, amene anali ndi chofukizira mʼmanja mwake wokonzeka kuti afukize lubani, anapsa mtima. Iye anakwiyira ansembewo. Ndipo ansembe aja akuona patsogolo pa guwa lofukizira lubani mʼNyumba ya Mulungu, khate linayamba pamphumi pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Uziya anapsa mtima, mbale ya zofukiza iri m'dzanja lace kufukiza nayo; ndipo pakupsa mtima nao ansembe, khate linabuka pamphumi pace, pamaso pa ansembe m'nyumba ya Yehova, pambali pa guwa lofukizapo.