2 Chronicles 26:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Azariya mkulu wa ansembe, pamodzi ndi ansembe onse atamuyang'ana, adangoona kuti wachita khate pa mphumi. Ansembewo adamkankhira kunja mwamsanga, ndipo iye mwini wake adatuluka msangamsanga, chifukwa chakuti Chauta adaamlanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Azariya wansembe wamkulu, ndi ansembe onse, anampenya, ndi kuona kuti anali wakhate pamphumi pake namkankhira msanga kubwalo; nafulumiranso yekha kutulukako, pakuti Yehova adamkantha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Azariya, mkulu wa ansembe pamodzi ndi ansembe ena onse atamuyangʼana anaona kuti anali ndi khate pamphumi pake, ndipo anamutulutsa mofulumira. Ndipo iye mwini anafulumira kutuluka, chifukwa Yehova anamulanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Azariya wansembe wamkulu, ndi ansembe onse, anampenya, ndi kuona kuti anali wakhate pamphumi pace namkankhiza msanga kubwalo; nafulumiranso yekha kuturukako, pakuti Yehova adamkantha.